Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 16:2 - Buku Lopatulika

2 Pamenepo Asa anatulutsa siliva ndi golide ku chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu; nazitumiza kwa Benihadadi mfumu ya Aramu, yokhala ku Damasiko, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pamenepo Asa anatulutsa siliva ndi golide ku chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu; nazitumiza kwa Benihadadi mfumu ya Aramu, yokhala ku Damasiko, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono Asa adatenga siliva ndi golide ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso ku nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, amene ankakhala ku Damasiko. Mau a Asa anali akuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo Asa anatenga siliva ndi golide ku malo osungirako a mʼNyumba ya Mulungu ndi ku nyumba yake yaufumu ndi kuzitumiza kwa Beni-Hadadi mfumu ya Aramu imene inkakhala mu Damasiko.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 16:2
8 Mawu Ofanana  

Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golide yense anatsala pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma chili m'nyumba ya Yehova chuma chili m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ake; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,


Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yehoramu, ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zakezake, ndi golide yense anampeza pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaele mfumu ya Aramu; motero anabwerera kuchoka ku Yerusalemu.


Natenga Ahazi siliva ndi golide wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asiriya.


Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu.


Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa, Baasa mfumu ya Israele anakwera kulimbana ndi Yuda, namangitsa Rama, kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.


Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, monga pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndakutumizirani siliva ndi golide; mukani, pasulani pangano lanu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere.


Pakuti Ahazi analandako za m'nyumba ya Yehova ndi za m'nyumba ya mfumu, ndi ya akalonga, nazipereka kwa mfumu ya Asiriya, osathandizidwa nazo.


Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa