Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 16:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo taonani, zochita Asa, zoyamba ndi zotsiriza, zalembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo taonani, zochita Asa, zoyamba ndi zotsiriza, zalembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono ntchito za Asa, kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, zidalembedwa m'buku la Mafumu a ku Yuda ndi a ku Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ntchito zina za mfumu Asa, kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto zalembedwa mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 16:11
11 Mawu Ofanana  

Machitidwe ake tsono a Rehobowamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku onse.


Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m'kaidi; pakuti adapsa naye mtima chifukwa cha ichi. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena.


Machitidwe ena tsono adazichita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wotchulidwa m'buku la mafumu a Israele.


Machitidwe ena tsono a Amaziya, oyamba ndi otsiriza, taonani, sanalembedwe kodi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele?


Machitidwe ena tsono a Uziya, oyamba ndi otsiriza, anawalemba Yesaya mneneri mwana wa Amozi.


Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zake zonse, ndi njira zake, taonani, zalembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda.


Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi ntchito zake zokoma, taonani, zilembedwa m'masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele.


Ndipo Safani mlembi anauza mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe anandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.


ndi zochita iye, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda.


Machitidwe ena tsono a Solomoni, oyamba ndi otsiriza, sanalembedwe kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobowamu mwana wa Nebati?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa