2 Mbiri 15:9 - Buku Lopatulika9 Namemeza onse a mu Yuda ndi mu Benjamini, ndi iwo akukhala nao ochokera ku Efuremu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ochuluka ochokera ku Israele, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wake anali naye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Namemeza onse a m'Yuda ndi m'Benjamini, ndi iwo akukhala nao ochokera ku Efuremu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ochuluka ochokera ku Israele, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wake anali naye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Adasonkhanitsa Ayuda onse ndi Abenjamini ndiponso anthu a ku Efuremu, Manase ndi Simeoni amene ankangokhala nao, pakuti anthu ambiri anali atathaŵira kwa mfumu Asa, kuchoka ku Israele, ataona kuti Chauta Mulungu wake anali naye Asayo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Kenaka anasonkhanitsa anthu onse a ku Yuda ndi Benjamini ndiponso anthu ochokera ku Efereimu, Manase ndi Simeoni amene ankakhala pakati pawo, pakuti gulu lalikulu linabwera kwa iye kuchokera ku Israeli litaona kuti anali ndi Yehova Mulungu wake. Onani mutuwo |