Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 14:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo anawatulukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi chikwi chimodzi, ndi magaleta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anawatulukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi chikwi chimodzi, ndi magaleta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Zera wa ku Etiopiya adanyamuka kukamenyana ndi Ayuda atatenga gulu lake lankhondo la anthu 1,000,000, ndi magaleta 300, ndipo adakafika mpaka ku Maresa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Zera wa ku Kusi anapita kukamenyana nawo ali ndi gulu lalikulu kwambiri la asilikali ndi magaleta 300 ndipo anafika mpaka ku Maresa.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 14:9
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, watuluka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti,


ndi Gati, ndi Maresa, ndi Zifi,


Natuluka Asa pamaso pake, nanika nkhondoyi m'chigwa cha Zefati ku Maresa.


Nanga Akusi ndi Alibiya, sanakhale khamu lalikulukulu, ndi magaleta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m'dzanja mwanu?


limene litumiza mithenga pamtsinje m'ngalawa zamagumbwa zoyenda m'madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msangamsanga kumtundu wa anthu aatali ndi osalala, kwa mtundu woopsa chikhalire chao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa!


Kusi, ndi Puti, ndi Ludi, ndi osokonezeka onse, ndi Libiya, ndi anthu a dziko lopangana nao, adzagwa pamodzi nao ndi lupanga.


Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israele? Ati Yehova. Sindinakweza Israele ndine, kumtulutsa m'dziko la Ejipito, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?


Ndidzakutengeranso wokhala mu Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale cholowa chake; ulemerero wa Israele udzafikira ku Adulamu.


ndi Keila ndi Akizibu, ndi Maresa; mizinda isanu ndi inai pamodzi ndi midzi yao.


pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa