2 Mbiri 14:1 - Buku Lopatulika1 Momwemo Abiya anagona ndi makolo ake, ndipo anamuika m'mzinda wa Davide; ndi Asa mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake; m'masiku ake dziko linaona bata zaka khumi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Momwemo Abiya anagona ndi makolo ake, ndipo anamuika m'mudzi wa Davide; ndi Asa mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake; m'masiku ake dziko linaona bata zaka khumi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Tsono Abiya adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Pambuyo pake Asa mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Pa masiku a Asa, dziko lidakhala pa mtendere zaka khumi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Tsono Abiya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide. Asa mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake ndipo pa masiku ake, dziko linakhala pa mtendere kwa zaka khumi. Onani mutuwo |