2 Mbiri 13:9 - Buku Lopatulika9 Simunapirikitse kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amachita anthu a m'maiko ena? Kuti aliyense wakudza kudzipatulira ndi mwanawang'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Simunapirikitsa kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amachita anthu a m'maiko ena? Kuti aliyense wakudza kudzipatulira ndi mwanawang'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Kodi inu simudapirikitsa ansembe a Chauta, ana a Aaroni, ndiponso Alevi, ndipo mudadzisankhira ansembe anuanu, monga amachitira anthu a mitundu ina am'maikomo? Munthu aliyense amene amabwera kuti adzipereke atatenga mwanawang'ombe wamphongo kapena nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, amasanduka wansembe wa zinthu zimene sizili milungu konse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Koma kodi inu simunathamangitse ansembe a Yehova, ana a Aaroni ndiponso Alevi ndi kudzisankhira ansembe anuanu monga anthu ena amachitira? Aliyense amene amabwera kuti adzipatule atatenga mwana wangʼombe wamwamuna ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri amakhala wansembe wa zinthu zimene sizili milungu. Onani mutuwo |