Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 13:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu anaang'ombe agolide adawapanga Yerobowamu akhale milungu yanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu anaang'ombe agolide adawapanga Yerobowamu akhale milungu yanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 “Tsopano inu mukuganiza zolimbana ndi ufumu wa Chauta ndi kuulanda m'manja mwa ana a Davide, poti inuyo ndinu ambirimbiri. Ndipo muli nawo mafano agolide, a anaang'ombe amene Yerobowamu adakupangirani, kuti akhale milungu yanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Ndipo tsopano inu mwakonzekera kutsutsana ndi ufumu wa Yehova, umene uli mʼmanja mwa zidzukulu za Davide. Inu ndithu mulipo ankhondo ambirimbiri ndipo muli ndi ana angʼombe agolide amene Yeroboamu anapanga kuti akhale milungu yanu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 13:8
15 Mawu Ofanana  

Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito.


Ndipo anaimika mmodzi ku Betele, naimika wina ku Dani.


koma wachimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu ina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako;


nadziikira ansembe a misanje, ndi a ziwanda, ndi a anaang'ombe adawapanga.


Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.


nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa mu Mwamba kodi? Sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? Ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulimbana ndi Inu.


Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wake, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ake; popeza Mulungu wanu anakonda Aisraele kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kuchita chiweruzo ndi chilungamo.


Palibe mfumu yoti gulu lalikulu limpulumutsa, mphamvu yaikulu siichilanditsa chiphona.


Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa