Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 12:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Sisake mfumu ya Aejipito anakwerera Yerusalemu, nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; anazichotsa zonse; anachotsanso zikopa zagolide adazipanga Solomoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Sisake mfumu ya Aejipito anakwerera Yerusalemu, nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; anazichotsa zonse; anachotsanso zikopa zagolide adazipanga Solomoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono Sisake, mfumu ya ku Ejipito, adabwera kudzathira Yerusalemu nkhondo. Adalanda chuma cha ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi chuma cha ku nyumba ya mfumu. Adatenga zonse, ngakhalenso zishango zomwe zagolide zimene Solomoni adaapanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Sisaki mfumu ya dziko la Igupto atathira nkhondo Yerusalemu, iye anatenga chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu. Iye anatenga zinthu zonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomoni anapanga.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 12:9
8 Mawu Ofanana  

Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golide yense anatsala pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma chili m'nyumba ya Yehova chuma chili m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ake; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,


Natenga Ahazi siliva ndi golide wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asiriya.


Ndipo Rehobowamu mfumu anapanga m'malo mwa izi zikopa zamkuwa, nazipereka m'manja mwa kapitao wa olindirira akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.


Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse; pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika, amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa