2 Mbiri 12:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzichepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzichepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa chipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzichepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzichepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa chipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Tsono Chauta ataona kuti anthuwo adzichepetsa, adauzanso Semaya kuti, “Anthuŵa adzichepetsa, sindidzaŵaononga ai, koma ndidzaŵapulumutsa. Sindidzaukwiyira mzinda wa Yerusalemu, motero Sisake sadzauwononga konse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Yehova ataona kuti adzichepetsa, anayankhula ndi Semaya kuti, “Pakuti adzichepetsa, Ine sindiwawononga koma posachedwapa ndiwapulumutsa. Sinditsanulira ukali wanga pa Yerusalemu kudzera mwa Sisaki. Onani mutuwo |