Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 12:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo pakudzichepetsa iye mkwiyo wa Yehova unamchokera, kuti usamuononge konse; ndiponso munatsalira zokoma mu Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo pakudzichepetsa iye mkwiyo wa Yehova unamchokera, kuti usamuononge konse; ndiponso munatsalira zokoma m'Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsono mfumuyo itadzichepetsa, Chauta adaleka kufuna kuŵaononga kwathunthu. Motero zinthu zinkayenda bwino ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pakuti mfumu Rehobowamu inadzichepetsa, mkwiyo wa Yehova unamuchokera, sanawonongedweretu. Kunena zoona, munali zinthu zina zabwino mu Yuda.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 12:12
12 Mawu Ofanana  

Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mzinda; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?


Ndipo Aisraele onse adzamlira, nadzamuika, popeza iye yekha wa ana a Yerobowamu adzalowa m'manda; pakuti mwa iye mwapezedwa chokoma cha kwa Yehova Mulungu wa Israele m'nyumba ya Yerobowamu.


Ndipo kunatero kuti pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, anadza olindirira, nazinyamula, nazibwezanso ku chipinda cha olindirira.


Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazichotsa zifanizo m'dzikomo, mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake.


Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka,


Pakuti samasautsa dala, ngakhale kumvetsa ana a anthu chisoni.


Ife tilakwa ndi kupikisana nanu, ndipo Inu simunatikhululukire.


Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa