2 Mbiri 12:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo kunachitika, utakhazikika ufumu wa Rehobowamu, nalimbika iye, anasiya chilamulo cha Yehova, ndi Aisraele onse pamodzi naye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo kunachitika, utakhazikika ufumu wa Rehobowamu, nalimbika iye, anasiya chilamulo cha Yehova, ndi Aisraele onse pamodzi naye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Rehobowamu atangokhazikitsa ulamuliro wake ndi kuulimbitsa, iyeyo pamodzi ndi Aisraele onse adayamba kusiya malamulo a Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Rehobowamu atakhazikika monga mfumu nakhaladi wamphamvu, iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse anasiya malamulo a Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri mu Yerusalemu, m'mzinda m'mene Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele kukhazikamo dzina lake. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni.
Nadzilimbitsa Rehobowamu mfumu mu Yerusalemu, nachita ufumu; pakuti Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri mu Yerusalemu, ndiwo mzinda Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele, kuikapo dzina lake; ndipo dzina la make ndiye Naama Mwamoni.