Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 11:4 - Buku Lopatulika

4 Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense kunyumba yake; pakuti chinthu ichi chifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobowamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense kunyumba yake; pakuti chinthu ichi chifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobowamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 ‘Ine Chauta ndikuti, Musapite kukamenyana ndi abale anu. Aliyense abwerere kwao, poti zimene zachitikazi zachokera kwa Ine.’ ” Anthuwo adamvera mau a Chauta, nadabwerera osapita kukamenyana ndi Yerobowamu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 ‘Yehova akuti: Musapite kukamenyana ndi abale anu. Pitani kwanu, aliyense wa inu, pakuti izi ndikuchita ndine.’ ” Choncho anamvera mawu a Yehova ndi kubwerera osapita kukamenyana ndi Yeroboamu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 11:4
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale.


Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.


Pomwepo Abinere anaitana Yowabu nati, Kodi lupanga lidzaononga chionongere? Sudziwa kodi kuti kutha kwake kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao?


Ndipo mfuu unafikira khamu lonse la nkhondo polowa dzuwa, ndi kuti, Yense kumzinda kwao, ndi yense ku dziko la kwao.


Lankhula ndi Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda ndi Benjamini, ndi kuti,


Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire, zolingirira za m'mtima mwake ku mibadwomibadwo.


Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe.


Ndipo m'mawa mwake anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; muchitirana choipa bwanji?


Chikondi cha pa abale chikhalebe.


Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa