Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 11:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo anachita mwanzeru, nabalalitsa ana ake aamuna onse m'maiko onse a Yuda ndi Benjamini, kumizinda yonse yamalinga; nawapatsa chakudya chochuluka, nawafunira akazi ochuluka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo anachita mwanzeru, nabalalitsa ana ake amuna onse m'maiko onse a Yuda ndi Benjamini, kumidzi yonse yamalinga; nawapatsa chakudya chochuluka, nawafunira akazi ochuluka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Tsono mwanzeru adaika ena mwa ana ake aamuna m'zigawo zonse za ku Yuda ndi za ku Benjamini, ku mizinda yonse yamalinga. Ankaŵapatsa chakudya chambiri ndi kuŵafunira akazi ochuluka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Iye anachita mwanzeru, pomwaza ena mwa ana ake ku madera onse a Yuda ndi Benjamini, ndi ku mizinda yonse yotetezedwa. Iye anawapatsa zinthu zambiri ndiponso anawafunira akazi ambiri.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 11:23
8 Mawu Ofanana  

Koma kwa ana a akazi ake aang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isaki mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa.


Ndipo Rehobowamu anaika Abiya mwana wa Maaka akhale wamkulu, kalonga mwa abale ake; ndiko kuti adzamlonga ufumu.


Ndipo Rehobowamu anakhala mu Yerusalemu, namanga mizinda yolimbikiramo mu Yuda.


Ndipo kunachitika, utakhazikika ufumu wa Rehobowamu, nalimbika iye, anasiya chilamulo cha Yehova, ndi Aisraele onse pamodzi naye.


Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikulu, zasiliva, ndi zagolide, ndi za mtengo wake, pamodzi ndi mizinda yamalinga mu Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wake woyamba.


Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa