Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 11:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m'mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m'mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono anthu amene adatsimikiza mumtima mwao kuti azitumikira Chauta, Mulungu wa Israele, ankatsatira ansembe ndi Alevi aja, kuchoka ku mafuko a ku Israele, kupita ku Yerusalemu kukapereka nsembe kwa Chauta, Mulungu wa makolo ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Anthu ochokera fuko lililonse la Israeli amene anatsimikiza mitima yawo kufunafuna Yehova Mulungu wa Israeli, ankapitabe ku Yerusalemu kukapereka nsembe kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 11:16
28 Mawu Ofanana  

Mchitireni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani pamaso pake; lambirani Yehova m'chiyero chokometsetsa.


Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israele.


Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la chipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, kunyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.


Momwemo analimbikitsa ufumu wa Yuda, nalimbikitsa Rehobowamu, mwana wa Solomoni zaka zitatu; pakuti anayenda m'njira ya Davide ndi Solomoni zaka zitatu.


Nalowa chipangano chakufuna Yehova Mulungu wa makolo ao ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse;


Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi khumbo lao lonse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.


Namemeza onse a mu Yuda ndi mu Benjamini, ndi iwo akukhala nao ochokera ku Efuremu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ochuluka ochokera ku Israele, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wake anali naye.


Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazichotsa zifanizo m'dzikomo, mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.


Ndipo Yehosafati anachita mantha, nalunjikitsa nkhope yake kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.


Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anachokera kumizinda yonse ya Yuda kufuna Yehova.


Komatu ena a Asere ndi Manase ndi a Zebuloni anadzichepetsa, nadza ku Yerusalemu.


Akadzikumbukira yekha mumtima mwake, akadzisonkhanitsira yekha mzimu wake ndi mpweya wake,


Wakhazikika mtima wanga, Mulungu; ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.


Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.


koma iyeyu wosasamalira mau a Yehova anasiya anyamata ndi zoweta zake kubusa.


Ndipo mfumu m'mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wake pa Daniele kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa.


Adyerera tchimo la anthu anga, nakhumbira chosalungama chao, yense ndi mtima wake.


Chifukwa chake tsono, atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.


ndi okhala m'mzinda umodzi adzamuka kumzinda wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso.


ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;


Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.


nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikuchitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mau onse a chilamulo ichi.


Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m'dziko la cholowa cha Yehova m'mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa