Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 11:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo ansembe ndi Alevi okhala mu Israele yense anadziphatikiza kwa iye, ochokera m'malire ao onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo ansembe ndi Alevi okhala m'Israele lonse anadziphatikiza kwa iye, ochokera m'malire ao onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ansembe pamodzi ndi Alevi amene anali m'dziko lonse la Israele adatsata Rehobowamu, kuchoka konse kumene ankakhala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ansembe ndi Alevi a mʼmadera onse a Israeli anakhala mbali ya Rehobowamu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 11:13
11 Mawu Ofanana  

Koma ana aja a Israele akukhala m'mizinda ya Yuda, Rehobowamu anakhalabe mfumu yao.


Ndipo Baasa mfumu ya Israele anakwera ndi nkhondo ku Yuda, namanga ku Rama kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.


Ndipo anadza munthu kuchokera ku Baala-Salisa, nabwera nayo m'thumba mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye.


Ndi m'mizinda iliyonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa chilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ake.


Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko aoao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobowamu ndi ana ake anawataya, kuti asachitire Yehova ntchito ya nsembe;


Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa, Baasa mfumu ya Israele anakwera kulimbana ndi Yuda, namangitsa Rama, kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.


Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m'mizinda yonse ya Yuda, ndi akulu a nyumba za makolo mu Israele; nadza iwo ku Yerusalemu.


Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israele ndi Yuda onse, nalembanso makalata kwa Efuremu ndi Manase, kuti abwere kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska.


Koma ngati muti, Katundu wa Yehova, chifukwa chake Yehova atero: Chifukwa muti mau awa, Katundu wa Yehova, ndipo ndatuma kwa inu, kuti, Musati, Katundu wa Yehova;


Dzichenjerani nokha, musataye Mlevi masiku onse akukhala inu m'dziko mwanu.


Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m'dziko la cholowa cha Yehova m'mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa