Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 11:12 - Buku Lopatulika

12 Ndi m'mizinda iliyonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa chilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndi m'midzi iliyonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa chilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Adaikamo zishango ndi mikondo, ndipo adaitchinjiriza kwambiri mizindayo. Choncho ankalamulira anthu a ku Yuda ndi a ku Benjamini.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mʼmizinda yonse anayikamo zishango zikuluzikulu ndi mikondo, ndipo anachititsa kuti mizindayo ikhale yamphamvu. Choncho iye amalamulira Yuda ndi Benjamini.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 11:12
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pake, nang'amba chovala cha mawangamawanga chimene analikuvala, nagwira dzanja lake pamutu pake, namuka nayenda, nalira komveka.


Ndipo Abisalomu sanalankhule ndi Aminoni chabwino kapena choipa, pakuti Abisalomu anamuda Aminoni popeza adachepetsa mlongo wake Tamara.


Koma za ana a Israele okhala m'mizinda ya Yuda, Rehobowamu anakhalabe mfumu yao.


Ndipo analimbitsa malingawo, naikamo atsogoleri, ndi chakudya chosungikiratu, ndi mafuta, ndi vinyo.


Ndipo ansembe ndi Alevi okhala mu Israele yense anadziphatikiza kwa iye, ochokera m'malire ao onse.


ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.


Ndipo Yehosafati anakula chikulire, namanga mu Yuda nyumba zansanja, ndi mizinda ya chuma.


Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m'mzinda wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka.


Tsono, iwe wobadwa ndi munthu, Tenga mtengo umodzi, nulembepo, Wa Yuda ndi wa ana a Israele anzake; nutenge mtengo wina, nulembepo, Wa Yosefe, mtengo wa Efuremu, ndi wa nyumba yonse ya Israele anzake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa