Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 11:10 - Buku Lopatulika

10 ndi Zora, ndi Ayaloni, ndi Hebroni; ndiyo mizinda yamalinga ya mu Yuda ndi Benjamini.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 ndi Zora, ndi Ayaloni, ndi Hebroni; ndiyo midzi yamalinga ya m'Yuda ndi Benjamini.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Zora, Aiyaloni ndi Hebroni. Mizinda yamalinga yonseyo inali ku Yuda ndi ku Benjamini.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Zora, Ayaloni ndi Hebroni. Iyi ndiye inali mizinda yotetezedwa ya Yuda ndi Benjamini.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 11:10
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Sara anafa mu Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.


Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mizinda wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni.


Ndipo Davide anali mfumu ya nyumba ya Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi.


Ndipo analimbitsa malingawo, naikamo atsogoleri, ndi chakudya chosungikiratu, ndi mafuta, ndi vinyo.


ndi Adoraimu, ndi Lakisi, ndi Azeka,


Afilisti omwe adagwa m'mizinda ya kuchidikha, ndi ya kumwera kwa Yuda, nalanda Betesemesi, ndi Ayaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi midzi yake, ndi Timna ndi midzi yake, ndi Gimizo ndi midzi yake; nakhala iwo komweko.


Ndipo anakwera njira ya kumwera nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talimai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zowani mu Ejipito.)


Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele; ndipo anati pamaso pa Israele, Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni, ndi Mwezi iwe, m'chigwa cha Ayaloni.


Ndipo Yoswa ndi Aisraele onse naye anakwera kuchokera ku Egiloni mpaka ku Hebroni, nauthira nkhondo;


Chifukwa chake Hebroni likhala cholowa chake cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi mpaka lero lino; popeza anatsata Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wonse.


Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.


Ku chigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina;


Ndipo anapatula Kedesi mu Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa