Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 10:8 - Buku Lopatulika

8 Koma analeka uphungu wa akuluakuluwa adampangirawo, nakafunsana ndi anyamata anakula naye pamodzi, oimirira pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma analeka uphungu wa akulu akuluwa adampangirawo, nakafunsana ndi anyamata anakula naye pamodzi, oimirira pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma Rehobowamu adanyozera zimene madoda aja adaamlangiza nakapempha nzeru kwa achinyamata anzake amene adaakula naye pamodzi namamtumikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakulu anamupatsa ndipo anakafunsira nzeru kwa anyamata amene anakula naye pamodzi komanso amamutumikira.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 10:8
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.


Nati nao, Mundipangire bwanji inu, kuti tibwezere mau anthu awa ananena nanewo, ndi kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenzetsa ife?


koma munapeputsa uphungu wanga wonse, ndi kukana kudzudzula kwanga.


Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.


Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.


Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.


Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.


Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake; ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira.


Tsoka kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana, ndipo akalonga ako adyera mamawa!


Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere tchimo ndi tchimo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa