Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 10:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Rehobowamu mfumu anafunsana ndi akuluakulu, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake akali ndi moyo, nati, Mundipangire bwanji, kuti ndiwabwezere mau anthu awa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Rehobowamu mfumu anafunsana ndi akuluakulu, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake akali ndi moyo, nati, Mundipangire bwanji, kuti ndiwabwezere mau anthu awa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono mfumu Rehobowamu adapempha nzeru kwa madoda amene ankakhala ndi bambo wake Solomoni ndi kumamlangiza akali moyo. Adaŵafunsa kuti, “Inu mungandilangize zotani kuti ndiŵayankhe anthu ameneŵa?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kenaka mfumu Rehobowamu anafunsira nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira abambo ake, Solomoni, pamene anali moyo. Iye anafunsa kuti, “Kodi inu mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu awa?”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 10:6
11 Mawu Ofanana  

Pomwepo Abisalomu ananena ndi Ahitofele, Upangire chimene ukuti tikachite.


Ndipo ananena nao, Mubwerenso atapita masiku atatu. Nachoka anthu.


Ndinati, Amisinkhu anene, ndi a zaka zochuluka alangize nzeru.


Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake; koma wanzeru amamvera uphungu.


Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.


Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.


Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzachita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa