Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 10:4 - Buku Lopatulika

4 Atate wanu analemeretsa goli lathu; inu tsono pepuzaniko ntchito yolemetsa ya atate wanu, ndi goli lake lolemera anatisenzetsali, ndipo tidzakutumikirani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Atate wanu analemeretsa goli lathu; inu tsono pepuzaniko ntchito yolemetsa ya atate wanu, ndi goli lake lolemera anatisenzetsali, ndipo tidzakutumikirani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 “Bambo wanu ankatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri. Ndiye ife tikuti inu tsopano mudzatipeputsireko goli lolemetsalo ndi ntchito zoŵaŵa zimene bambo wanu adatisenzetsa, apo ife tidzakutumikirani.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma tsopano mutipeputsire ntchito yolemetsayi ndi goli lolemerali limene analiyika pa ife ndipo ifeyo tidzakutumikirani.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 10:4
15 Mawu Ofanana  

Atate wanu analemeretsa goli lathu, ndipo inu tsono pepuzaniko ntchito zosautsa za atate wanu, ndi goli lolemera lake limene anatisenza, ndipo tidzakutumikirani.


Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.


Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.


Ndipo mfumu Solomoni anasonkhetsa athangata mwa Aisraele onse, ndi athangatawo ndiwo anthu zikwi makumi atatu.


Ndipo Solomoni anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m'mapiri;


Koma Solomoni sanawayese ana a Israele akapolo, koma iwowo anali anthu a nkhondo, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi akazembe ake, ndi oyang'anira magaleta ake ndi apakavalo ake.


Ndipo anatuma munthu kukamuitana, nadza Yerobowamu ndi Aisraele onse, nalankhula ndi Rehobowamu, ndi kuti,


Ndipo ananena nao, Mubwerenso atapita masiku atatu. Nachoka anthu.


Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.


Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsere chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.


Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chao.


Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa