Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 10:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo kunali, atamva Yerobowamu mwana wa Nebati (popeza anali mu Ejipito kumene adathawira, kuthawa Solomoni mfumu), Yerobowamu anabwera kuchoka ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo kunali, atamva Yerobowamu mwana wa Nebati (popeza anali m'Ejipito kumene adathawira, kuthawa Solomoni mfumu), Yerobowamu anabwera kuchoka ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu, mwana wa Nebati, ali ku Ejipito, momwe adaathaŵira mfumu Solomoni muja. Tsono atamva zaufumuzo, adachokako ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yeroboamu mwana wa Nebati atamva zimenezi (Iye anali ku Igupto, kumene anapita pothawa mfumu Solomoni) anabwerako kuchokera ku Igupto.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 10:2
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Yerobowamu mwana wa Nebati Mwefuremu wa ku Zereda mnyamata wa Solomoni, dzina la amake ndiye Zeruya, mkazi wamasiye, iyenso anakweza dzanja lake pa mfumu.


Ndipo munthu ameneyo Yerobowamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomoni anamuona mnyamatayo kuti ngwachangu, anamuika akhale woyang'anira wa ntchito yonse ya nyumba ya Yosefe.


Chifukwa chake Solomoni anafuna kupha Yerobowamu, ndipo Yerobowamu anathawira ku Ejipito kwa Sisake mfumu ya Aejipito, nakhala mu Ejipito kufikira imfa ya Solomoni.


Ndipo kunali kuti Yerobowamu mwana wa Nebati anachimva akali mu Ejipito, kumene anathawira kuchokera ku maso a Solomoni mfumu, pakuti Yerobowamu anakhala ku Ejipito.


Ndipo anatuma munthu kukamuitana, nadza Yerobowamu ndi Aisraele onse, nalankhula ndi Rehobowamu, ndi kuti,


Machitidwe ena tsono a Solomoni, oyamba ndi otsiriza, sanalembedwe kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobowamu mwana wa Nebati?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa