2 Mbiri 10:16 - Buku Lopatulika16 Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu sinawamvere anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu, Aisraele inu; yang'anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisraele onse anamuka ku mahema ao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu sinawamvera anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu, Aisraele inu; yang'anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisraele onse anamuka ku mahema ao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Tsono Aisraele onsewo ataona kuti mfumu sidamvere zimene ankapemphazo, adayankha kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanjinso m'banja la Davide? Sitingayembekeze choloŵa chilichonse m'banja la mwana wa Yese. Ndiye inu Aisraele, bwererani kumahema kwanu. Tsopano iwe mwana wa Davide, udziwonere wekha pa banja lako.” Choncho Aisraele onsewo adachoka napita ku nyumba zao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Aisraeli onse ataona kuti mfumu yakana kuwamvera, iwo anayankha mfumu kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanji mwa Davide, gawo lanji mwa mwana wa Yese? Inu Aisraeli! Pitani kwanu. Iwe Davide! Yangʼana banja lako.” Kotero Aisraeli onse anapita kwawo. Onani mutuwo |