Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 1:9 - Buku Lopatulika

9 Tsopano, Yehova Mulungu, likhazikike lonjezano lanu la kwa Davide atate wanga; pakuti mwandiika mfumu ya anthu akuchuluka ngati fumbi lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Tsopano, Yehova Mulungu, likhazikike lonjezano lanu la kwa Davide atate wanga; pakuti mwandiika mfumu ya anthu akuchuluka ngati fumbi lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Inu Chauta, zimene mudalonjeza kwa bambo wanga Davide zichitikedi, pakuti mwandiika kuti ndikhale mfumu yolamulira anthu ochuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Tsopano Inu Yehova Mulungu, lolani kuti lonjezo lanu kwa abambo anga Davide likwaniritsidwe, pakuti mwandiyika kukhala mfumu ya anthu anu amene ndi ochuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 1:9
14 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.


kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;


mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.


ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana aamuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele.


Adzawerenga ndani fumbi la Yakobo, kapena kuwerenga limodzi la magawo anai la Israele? Ndipo ine ndife monga amafa oongoka mtima, chitsiriziro changa chifanane nacho chake!


Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa