Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 1:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo, nakhala nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'mizinda ya magaleta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo, nakhala nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magaleta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Adasonkhanitsa magaleta ndiponso anthu okwera pa akavalo. Magaletawo anali nawo 1,400, anthu okwera pa akavalo analipo 12,000. Adaŵakhazika ena ku mizinda yokhalako ankhondo ena pafupi ndi mfumu ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndi akavalo 12,000, amene anawayika mʼmizinda yosungira magaleta ndipo ena anali ndi iye mu Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 1:14
8 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri zagolide wonsansantha, chikopa chimodzi chinapangidwa ndi masekeli mazana asanu ndi limodzi.


Ndipo Solomoni anali nazo zipinda za akavalo a magaleta ake zikwi khumi mphambu ziwiri.


Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebanoni, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni.


ndi mizinda yonse yosungamo zinthu zake za Solomoni, ndi mizinda yosungamo magaleta ake, ndi mizinda yokhalamo apakavalo ake, ndi zina zilizonse zidakomera Solomoni kuzimanga mu Yerusalemu, ndi ku Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.


ndi Baalati, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi mizinda yonse ya magaleta ake, ndi mizinda ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa mu Yerusalemu, ndi mu Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.


Ndipo Solomoni anali nazo zipinda zikwi zinai za akavalo ndi magaleta, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'mizinda ya magaleta, ndi mu Yerusalemu kwa mfumu.


Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa