Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 9:7 - Buku Lopatulika

7 Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere chilango cha mwazi wa atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere chilango cha mwazi wa atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono mukakanthe banja la Ahabu mbuyanu, kuti Chautayo alipsire Yezebele, chifukwa cha aneneri ake ndiponso atumiki ena onse amene iyeyo adaŵapha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Uyenera kuwononga nyumba ya mbuye wako Ahabu ndipo ndidzabwezera imfa ya atumiki anga, aneneri ndiponso imfa ya atumiki ena onse a Yehova amene anaphedwa ndi Yezebeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 9:7
21 Mawu Ofanana  

pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.


Ndipo kunali, atamva Yezebele kuti anamponya Naboti miyala nafa, Yezebele anati kwa Ahabu, Taukani, landirani munda wampesa wa Naboti Myezireele uja anakana kukugulitsani ndi ndalama, popeza Naboti sali ndi moyo, koma wafa.


Taona, ndidzakufikitsira choipa, ndi kuchotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka mu Israele;


Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza.


Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba ya Ahabu; pakuti Yehova wachita chimene adanena mwa mtumiki wake Eliya.


Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu mu Yezireele, ndi omveka ake onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ake, mpaka sanatsale wa iye ndi mmodzi yense.


Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehoramu; pakuti atafika anatulukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.


kumvera mau a atumiki anga aneneri, amene ndituma kwa inu, pouka mamawa ndi kuwatuma iwo, koma simunamvere;


kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa padziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira kumwazi wa Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe.


Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.


pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.


Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.


Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake; adzalipsira mwazi wa atumiki ake, adzabwezera chilango akumuukira, nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake.


pakuti timdziwa Iye amene anati, Kubwezera chilango nkwanga, Ine ndidzabwezera. Ndiponso, Ambuye adzaweruza anthu ake.


Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.


pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.


Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa