Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 9:5 - Buku Lopatulika

5 Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndili ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa inu, kazembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndili ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa inu, kazembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Atafika, adapeza atsogoleri ankhondo ali pa msonkhano. Tsono iyeyo adati, “Zikomo bwana, ine ndili ndi mau oti ndikuuzeni.” Yehu adafunsa kuti, “Kodi ukunena yani mwa ifeyo?” Mneneri uja adayankha nati, “Inuyo bwana.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Atafika ku Giliyadiko anapeza atsogoleri a ankhondo ali pa msonkhano. Iye anati, “Mtsogoleri, ine ndili ndi uthenga wanu.” Ndipo Yehu anafunsa kuti, “Uthengawo ndi wa yani pakati pathu?” Mneneriyo anayankha kuti, “Ndi wa inuyo, mtsogoleri.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 9:5
4 Mawu Ofanana  

Ndipo ukafikako, ukaunguzeko Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi, nulowe numnyamukitse pakati pa abale ake, nupite naye ku chipinda cham'katimo.


Pamenepo mnyamatayo, ndiye mneneri, anamuka ku Ramoti Giliyadi.


Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pake, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisraele.


Koma iye mwini anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndili nao mau achinsinsi kwa inu, mfumu. Nati iye, Khalani chete. Ndipo anatuluka onse akuimapo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa