Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 9:34 - Buku Lopatulika

34 Ndipo atalowa, anadya namwa, nati, Kampenyeni tsono mkazi wotembereredwa uyu, nimumuike; popeza ndiye mwana wa mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ndipo atalowa, anadya namwa, nati, Kampenyeni tsono mkazi wotembereredwa uyu, nimumuike; popeza ndiye mwana wa mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Pambuyo pake Yehu adaloŵa m'nyumba yaufumu naadya ndi kumwa. Kenaka adati, “Kamtoleni mkazi wotembereredwa uja, mukamuike, pakuti ndi mwana wa mfumu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Yehu analowa mʼnyumba yaufumu ndipo anadya ndi kumwa. Kenaka iye anati, “Kamutoleni mkazi wotembereredwayo, ndipo kamuyikeni mʼmanda, popeza ndi mwana wa mfumu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 9:34
10 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m'machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikira Baala, namgwadira.


Ndipo Eliya ananena ndi Ahabu, Nyamukani, idyani, imwani; popeza kumveka mkokomo wa mvula yambiri.


Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza.


Nati iye, Mgwetsereni pansi. Namgwetsera pansi, nuwazikako mwazi wake pakhoma ndi pa akavalo, nampondereza iye pansi.


Namuka iwo kuti amuike; koma sanapezeko kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja.


Amtokoma anatuluka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m'chinyumba cha ku Susa; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mzinda wa Susa unadodoma.


Amayesa wolungama wodala pomkumbukira; koma dzina la oipa lidzavunda.


Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;


ogona pamakama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya anaankhosa a kuzoweta, ndi anaang'ombe ochoka pakati pa khola;


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa