2 Mafumu 9:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Munthu wokwera pa kavalo uja adapita kukakumana nawo nati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi ndi zamtendere?’ ” Yehu adayankha kuti, “Kodi iweyo nkhani ya mtendere uli nayo chiyani? Tiye, uzinditsata pambuyo.” Mlonda uja adakanena kwa mfumu Yoramu kuti, “Wamthenga uja wakafika ndithu kwa anthuwo, koma sakubwerako ai.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Choncho munthu wokwera kavalo anapita kukakumana ndi Yehu ndipo anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ” Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.” Mlonda uja anakafotokoza kwa mfumu kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwerera.” Onani mutuwo |