2 Mafumu 8:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zake zonse ndi zipatso zonse za m'munda, chichokere iye m'dziko mpaka lero lino. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zake zonse ndi zipatso zonse za m'munda, chichokere iye m'dziko mpaka lero lino. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Mfumu itamufunsa maiyo, iyeyo adaifotokozera kuti Elisa adaukitsadi mwana wake. Choncho mfumu ija idamuikira nduna maiyo niiwuza kuti, “Umbwezere zonse zimene zidaali zake, pamodzi ndi phindu lonse lochokera ku zokolola za kumunda kwake, kuyambira tsiku limene adachoka mpaka tsopano lino.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Mfumu inafunsa mayiyo za nkhaniyi ndipo iye anayifotokozera mfumuyo. Ndipo mfumu inasankha munthu woti ayendetse nkhani yake ndipo inati, “Mubwezereni zonse zimene zinali zake, kuphatikizapo phindu lonse lochokera mʼmunda wake, kuyambira tsiku limene anachoka mpaka tsopano lino.” Onani mutuwo |
Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.