Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 8:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo kunali, alimkufotokozera mfumu m'mene adamuukitsira wakufayo, taonani, mkaziyo adamuukitsira mwana wake ananena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu. Nati Gehazi, Mbuye wanga mfumu, suyu mkaziyo, suyu mwana wake Elisa anamuukitsayo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo kunali, alimkufotokozera mfumu m'mene adamuukitsira wakufayo, taonani, mkaziyo adamuukitsira mwana wake ananena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu. Nati Gehazi, Mbuye wanga mfumu, suyu mkaziyo, suyu mwana wake Elisa anamuukitsayo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pamene mtumikiyo ankauza mfumuyo m'mene Elisa adaukitsira anthu akufa, mkazi uja, amene mwana wake Elisa adamuukitsira, adadzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake. Pamenepo Gehazi adati, “Inu mbuyanga mfumu, pano pali mai, ndipo mwana wake ndi uyu amene Elisa adamuukitsa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pamene Gehazi ankayiwuza mfumuyo momwe Elisa anaukitsira anthu akufa, mayi amene mwana wake Elisa anamuukitsa kwa akufayo analowa kudzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake. Gehazi anati, “Mbuye wanga mfumu, mayi wake ndi uyu ndipo mwana wakeyo ndi uyu amene Elisa anamuukitsa kwa akufa.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 8:5
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magaleta; nakamangira Samariya misasa, naponyana nao nkhondo.


Nati kwa Gehazi mnyamata wake, Itana Msunamu uja. Namuitana, naima mkaziyo pamaso pake.


Pamenepo anabwera nayenda m'nyumba, chakuno kamodzi, chauko kamodzi; nakwera, nadzitambasuliranso pa iye; ndi mwana anayetsemula kasanu ndi kawiri, natsegula mwanayo maso ake.


Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo.


Ndipo popita mfumu ya Israele alikuyenda palinga, mkazi anamfuulira, nati, Ndithandizeni, mbuye wanga mfumu.


Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zake zonse ndi zipatso zonse za m'munda, chichokere iye m'dziko mpaka lero lino.


Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.


Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.


Mtima wa munthu ulingalira njira yake; koma Yehova ayendetsa mapazi ake.


Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.


Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?


Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ochekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Bowazi, ndiye wa banja la Elimeleki.


Ndipo Saulo anazindikira mau ake a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa