Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 8:18 - Buku Lopatulika

18 Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wake ndiye mwana wa Ahabu, nachita iye choipa pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wake ndiye mwana wa Ahabu, nachita iye choipa pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Tsono Yehoramuyo ankatsata makhalidwe oipa a mafumu a ku Aisraele, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, pakuti adaakwatira mwana wa Ahabu. Tsono ankachita zoipa zili zonse pamaso pa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Iye anatsatira khalidwe la mafumu a ku Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, popeza iye anakwatira mwana wa Ahabu. Yehoramu anachita zoyipa pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 8:18
21 Mawu Ofanana  

Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza.


Ndipo Yehosafati anachitana mtendere ndi mfumu ya Israele.


popeza anayenda m'njira ya mafumu a Israele, napititsanso mwana wake pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.


Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu chingwe choongolera cha Samariya, ndi chingwe cholungamitsira chilili cha nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuivundikira.


Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wake adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema chifanizo, monga anachita Ahabu mfumu ya Israele, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.


Ahaziya ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu chaka chimodzi. Ndi dzina la make ndiye Ataliya mdzukulu wa Omuri mfumu ya Israele.


Ndipo anayenda m'njira ya nyumba ya Ahabu, nachita choipa pamaso pa Yehova, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti ndiye wa chibale cha banja la Ahabu.


koma anafuna Mulungu wa kholo lake nayenda m'malamulo ake, osatsata machitidwe a Israele.


Yehosafati tsono anali nacho chuma ndi ulemu zomchulukira, nachita chibale ndi Ahabu.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israele, ndi kuchititsa Yuda ndi okhala mu Yerusalemu chigololo, monga umo anachitira chigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;


Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, umo mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wake; ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova.


Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa