Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 8:13 - Buku Lopatulika

13 Nati Hazaele, Koma nanga kapolo wanu ali chiyani, ndiye galu, kuti akachite chinthu chachikulu ichi? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Nati Hazaele, Koma nanga kapolo wanu ali chiyani, ndiye galu, kuti akachite chinthu chachikulu ichi? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Apo Hazaele adafunsa kuti, “Kodi kapolo wanune amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita zinthu zazikulu zoterezi?” Elisa adayankha kuti, “Chauta wandiwonetsa kuti iweyo udzakhala mfumu ya Asiriya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndipo Hazaeli anati, “Kodi kapolo wanune, amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita chinthu chachikulu chotere?” Elisa anayankha kuti, “Yehova wandionetsa kuti iwe udzakhala mfumu ya ku Aramu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 8:13
14 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya galu wakufa monga ine.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Bwerera ulendo wako, udzere kuchipululu kunka ku Damasiko, ndipo utafikako udzoze Hazaele akhale mfumu ya Aramu;


Ndipo Hazaele mfumu ya Aramu anapsinja Israele masiku onse a Yehowahazi.


Nanena naye Elisa, Kamuuze, kuti, Sudzachira konse; popeza Yehova wandionetsa kuti adzafa ndithu.


Pakuti andizinga agalu, msonkhano wa oipa wanditsekereza; andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.


Landitsani moyo wanga kulupanga; wokondedwa wanga kumphamvu ya galu,


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.


Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.


Penyererani agalu, penyererani ochita zoipa, penyererani choduladula;


Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.


Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine galu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide natchula milungu yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa