Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 8:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo anamyang'ana chidwi, mpaka anachita manyazi, nalira misozi munthu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo anamyang'ana chidwi, mpaka anachita manyazi, nalira misozi munthu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Atatero, Elisa adamuyang'ana kwambiri Hazaele mpaka adachita manyazi. Apo Elisayo adayamba kulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Elisa anamuyangʼana kwambiri Hazaeli mpaka anachita manyazi. Pamenepo munthu wa Mulungu anayamba kulira.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 8:11
15 Mawu Ofanana  

Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aejipito, ndipo anamva a m'nyumba ya Farao.


Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


Koma anamuumiriza kufikira anachita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza.


Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.


Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.


Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri.


Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


afulumire, atikwezere ife mau a maliro, kuti maso athu agwe misozi, ndi zikope zathu ziyendetse madzi.


Ndipo m'mene anayandikira, anaona mzindawo naulirira,


wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;


Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleke usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.


kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.


Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa