2 Mafumu 7:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo kunachitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa chipata cha Samariya; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo kunachitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa chipata cha Samariya; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Paja mneneri Elisa adaauza mfumu kuti, “Makilogramu asanu ndi limodzi a barele adzaŵagulitsa pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu atatu a ufa wosalala adzaŵagulitsanso pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva maŵa pa nthaŵi ngati yomwe ino ku chipata cha Samariya.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Zinachitika molingana ndi zomwe ananena munthu wa Mulungu zija kuti “Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.” Onani mutuwo |
Koma Elisa anakhala pansi m'nyumba mwake, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m'mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kuchotsa mutu wanga? Taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi chitseko. Kodi mapazi a mbuye wake samveka dididi pambuyo pake?