2 Mafumu 7:17 - Buku Lopatulika17 Koma mfumu idayang'anitsa pachipata kazembe amene uja idafotsamira padzanja lake; ndipo anthu anampondereza pachipata, nafa iye, monga umo adanenera munthu wa Mulungu, ponena paja anamtsikira mfumu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Koma mfumu idayang'anitsa pachipata kazembe amene uja idafotsamira pa dzanja lake; ndipo anthu anampondereza pachipata, nafa iye, monga umo adanenera munthu wa Mulungu, ponena paja anamtsikira mfumu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Pamene zinkachitika zimenezi, nkuti mfumu itaika phungu wake wokhulupirika uja kuti akhale wolamulira pa chipata. Koma anthu adapondereza phunguyo kuchipata kuja, kotero kuti adafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu adaanenera pamene mfumu idaapita kukamuwona. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Tsono mfumu inayika mtsogoleri amene ankamudalira uja kuti akhale woyangʼanira pa chipata ndipo anthu anamupondaponda ku chipata kuja, ndipo anafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu ananenera mfumu itapita ku nyumba yake. Onani mutuwo |
Koma Elisa anakhala pansi m'nyumba mwake, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m'mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kuchotsa mutu wanga? Taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi chitseko. Kodi mapazi a mbuye wake samveka dididi pambuyo pake?