Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 7:16 - Buku Lopatulika

16 Natuluka anthu, nafunkha m'misasa ya Aaramu. Ndipo anagula miyeso ya ufa ndi sekeli, nagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, monga umo adanenera Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Natuluka anthu, nafunkha m'misasa ya Aaramu. Ndipo anagula miyeso ya ufa ndi sekeli, nagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, monga umo adanenera Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono anthu a mu Samariya adatuluka nakafunkha ku zithando za Asiriya. Motero makilogramu atatu a ufa wosalala ankaŵagulitsadi pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu asanu ndi limodzi a barele ankaŵagulitsanso chimodzimodzi potsata m'mene adaanenera Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Tsono anthu a mu Samariya anatuluka nakafunkha ku msasa wa Aaramu. Kotero kuti makilogalamu atatu a ufa ankawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele ankawagulitsanso pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, monga momwe ananenera Yehova.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 7:16
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Elisa anati, Mverani mau a Yehova; atero Yehova, Mawa dzuwa lino adzagula muyeso wa ufa ndi sekeli, adzagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, pa chipata cha Samariya.


Ndipo anawalondola mpaka ku Yordani; ndipo taonani, m'njira monse munadzala ndi zovala ndi akatundu adazitaya Aaramu m'kufulumira kwao. Nibwera mithenga, nifotokozera mfumu.


Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka.


Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa, ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.


Pogona inu m'makola a zoweta, mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.


Tsoka kwa iwe amene usakaza, chinkana sunasakazidwe; nupangira chiwembu, chinkana sanakupangire iwe chiwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira chiwembu, iwo adzakupangira iwe chiwembu.


Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wake, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo cholanda chachikulu, chofunkha chinagawanidwa; wopunduka nafumfula.


Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga dzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo.


Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.


Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?


Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.


Ndipo ana a Israele atathamangira Afilisti, anabwerera nafunkha za m'zithando zao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa