Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 7:14 - Buku Lopatulika

14 Motero anatenga magaleta awiri ndi akavalo ao; ndipo mfumu inawatumiza alondole khamu la Aaramu, ndi kuti, Mukani mukaone.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Motero anatenga magaleta awiri ndi akavalo ao; ndipo mfumu inawatumiza alondole khamu la Aaramu, ndi kuti, Mukani mukaone.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Motero adasankha anthu aŵiri okwera pa akavalo, ndipo mfumuyo idaŵatuma kuti akalondole gulu la ankhondo la Asiriya. Idati, “Pitani mukaone chimene chachitika.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Choncho anasankha magaleta awiri pamodzi ndi akavalo ake, ndipo mfumu inawatuma kuti alondole gulu lankhondo la Aaramu. Mfumuyo inalamula oyendetsa akavalowo kuti, “Pitani kaoneni.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 7:14
3 Mawu Ofanana  

Nayankha mmodzi wa anyamata ake, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m'mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israele otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israele otsirizika; tiwatumize tione.


Ndipo anawalondola mpaka ku Yordani; ndipo taonani, m'njira monse munadzala ndi zovala ndi akatundu adazitaya Aaramu m'kufulumira kwao. Nibwera mithenga, nifotokozera mfumu.


Ndipo mlonda ali chilili pachilindiro mu Yezireele, naona gulu la Yehu lilinkudza, nati, Ndiona gulu. Nati Yoramu, Tenga wapakavalo, numtumize akomane nao, nanene, Mtendere kodi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa