Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 7:13 - Buku Lopatulika

13 Nayankha mmodzi wa anyamata ake, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m'mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israele otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israele otsirizika; tiwatumize tione.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Nayankha mmodzi wa anyamata ake, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m'mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israele otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israele otsirizika; tiwatumize tione.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Koma mmodzi mwa nduna zake adati, “Anthu a mumzinda muno posachedwa adzatsirizikanso monga Aisraele onse amene afa kaleŵa. Ndiye ife tiyeni tisankhe ena kuti atenge akavalo asanu amene atsalawo, tiŵatume kuti akaone.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Mmodzi mwa atsogoleri ake ankhondo anayankha kuti, “Chonde uzani anthu ena atenge akavalo asanu amene atsala mu mzinda muno. Taonani, zomwe zingawachitikire zidzakhala zofanana ndi zomwe zingachitikire ena onse amene atsala. Inde iwo adzangokhala ngati Aisraeli ena onse amene awonongeka kale. Choncho tiyeni tiwatume akafufuze zomwe zachitika.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 7:13
7 Mawu Ofanana  

Pamenepo anyamata ake anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani chinthu chachikulu, simukadachichita kodi? Koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?


Akali chilankhulire nao, tapenyani, wamtsikira mthengayo; ndi mfumu inati, Taonani, choipa ichi chichokera kwa Yehova; ndilindiranjinso Yehova?


Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ake, Ndikufotokozereni m'mene Aaramu atichitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, natuluka m'misasa, nabisala kuthengo, ndi kuti, Pamene atuluka m'mzinda tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m'mzindamo.


Motero anatenga magaleta awiri ndi akavalo ao; ndipo mfumu inawatumiza alondole khamu la Aaramu, ndi kuti, Mukani mukaone.


Tikati, Tilowe m'mzinda, m'mzinda muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa.


Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mzinda, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.


Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala; pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa