2 Mafumu 7:12 - Buku Lopatulika12 Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ake, Ndikufotokozereni m'mene Aaramu atichitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, natuluka m'misasa, nabisala kuthengo, ndi kuti, Pamene atuluka m'mzinda tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m'mzindamo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ake, Ndikufotokozereni m'mene Aaramu atichitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, natuluka m'misasa, nabisala kuthengo, ndi kuti, Pamene atuluka m'mudzi tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m'mudzimo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Pamenepo mfumu idadzuka usiku nikauza nduna zake kuti, “Ndikuuzeni zimene Asiriya atikonzera. Iwowo akudziŵa kuti ife tili ndi njala. Nchifukwa chake atuluka m'zithando kuti akabisale ku thengo. Choncho tikangotuluka mumzinda muno, iwowo atigwira amoyo ndipo aloŵa mumzinda muno.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Mfumu inadzuka usiku ndipo inawuza atsogoleri ake a ankhondo kuti, “Ndikukuwuzani zimene Aaramu atichitira ife. Akudziwa kuti tikufa ndi njala; kotero achoka mu msasa wawo kukabisala kuthengo ndi kuti, ‘Iwowa atuluka ndithu, ndipo ife tidzawagwira amoyo ndi kulowa mu mzindamo.’ ” Onani mutuwo |