Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 6:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israele, ndi kuti, Muchenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israele, ndi kuti, Muchenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma mneneri Elisa adatumiza mau kwa mfumu ya ku Israele kuti, “Chenjerani ku malo akutiakutiŵa, poti Asiriya akukabisala kumeneko.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Munthu wa Mulungu anatumiza mawu kwa mfumu ya ku Israeli kuti “Musamale podutsa malo akuti, chifukwa Aaramu akupita kumeneko.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 6:9
15 Mawu Ofanana  

Ndipo taonani, mneneri anadza kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukulu wonse? Taonani, ndidzaupereka m'dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.


Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ichi ndidzapereka unyinji uwu waukulu m'dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.


Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wake ulikumuwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ichi.


Pamenepo anadza, namfotokozera munthu wa Mulungu. Nati iye, Kagulitse mafuta, ukabwezere mangawa ako, ndi zotsalapo zikusunge iwe ndi ana ako.


Pamenepo mfumu ya Israele inatumiza kumene munthu wa Mulungu anamuuzako ndi kumchenjeza; nadzisunga osapitako, kawirikawiri.


Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo.


Ndipo mfumu ya Aramu inalinkuchita nkhondo ndi Israele, nipangana ndi anyamata ake, kuti, Misasa yanga idzakhala pakutipakuti.


Apititsa pachabe ziwembu za ochenjera, kuti manja ao sangathe kuchita chopangana chao.


Yehova aphwanya upo wa amitundu, asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu.


Maso a Yehova atchinjiriza wodziwa; koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu.


Ndipo Yehova anandidziwitsa, ndipo ndinadziwa; ndipo wandisonyeza ine machitidwe ao.


Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.


Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa