Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 6:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo mfumu ya Aramu inalinkuchita nkhondo ndi Israele, nipangana ndi anyamata ake, kuti, Misasa yanga idzakhala pakutipakuti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo mfumu ya Aramu inalinkuchita nkhondo ndi Israele, nipangana ndi anyamata ake, kuti, Misasa yanga idzakhala pakutipakuti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Nthaŵi ina mfumu ya ku Siriya inkamenyana nkhondo ndi Aisraele. Ndipo idapangana ndi aphungu ake kuti, “Tikamange zithando zathu pa malo akutiakuti.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Tsono mfumu ya ku Aramu inali pa nkhondo ndi Israeli. Itakambirana ndi atsogoleri ake ankhondo inati, “Ndidzamanga misasa yanga pamalo akutiakuti.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 6:8
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magaleta; nakamangira Samariya misasa, naponyana nao nkhondo.


Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m'mene atilakira; koma tikaponyana nao kuchidikha, zedi tidzaposa mphamvu.


Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza mizinda ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda mu Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera mu Samariya. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.


Ndipo Aaramu ndi Aisraele anakhala chete zaka zitatu, osathirana nkhondo.


Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magaleta ake, niti, Musaponyana ndi anthu aang'ono kapena aakulu, koma ndi mfumu ya Israele yokha.


Ndipo zitatha izi, Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse, nakwera, namangira misasa Samariya.


Nati, Katole. Natambasula dzanja lake, naitenga.


Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israele, ndi kuti, Muchenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.


Uphungu utsimikiza zolingalira, ponya nkhondo utapanga upo.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa