Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 6:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo wina analinkudula mtengo nkhwangwa inagwa m'madzi; ndipo anafuula, nati, Kalanga ine mbuyanga! Popeza njobwereka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo wina analinkudula mtengo nkhwangwa inagwa m'madzi; ndipo anafuula, nati, Kalanga ine mbuyanga! Popeza njobwereka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Koma pamene wina ankagwetsa nsichi, nkhwangwa yake idaguluka nigwa m'madzi, ndipo adafuula kuti, “Kalanga ine mbuyanga! Ndipotu nkhwangwa imeneyi njobwereka!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pamene wina ankadula mtengo, nkhwangwa yake inaguluka nigwera mʼmadzi. Iye anafuwula kuti, “Mayo! Mbuye wanga! Popeza ndi yobwereka!”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 6:5
12 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu ya Israele inati, Kalanga ife! Pakuti Yehova waitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Mowabu.


Pamenepo anadza, namfotokozera munthu wa Mulungu. Nati iye, Kagulitse mafuta, ukabwezere mangawa ako, ndi zotsalapo zikusunge iwe ndi ana ako.


Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, natuluka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mzinda ndi akavalo ndi magaleta. Ndi mnyamata wake ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! Tichitenji?


Namuka nao, nafika ku Yordani, iwo natema mitengo.


Nati munthu wa Mulungu, Yagwera pati? Namuonetsapo yagwera. Pamenepo anadula kamtengo, nakaponya pomwepo, nayandamitsa nkhwangwayo.


Woipa akongola, wosabweza, koma wolungama achitira chifundo, napereka.


Chitsulo chikakhala chosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pochenjeza.


Ndipo adzadula nkhalango za m'thengo ndi chitsulo, ndipo Lebanoni adzagwa ndi wamphamvu.


chifukwa chakuopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, Babiloni, mzinda wolimba! Pakuti mu ora limodzi chafika chiweruziro chanu.


nadzanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukulu wovala bafuta ndi chibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golide ndi mwala wa mtengo wake, ndi ngale!


Ndipo anathira fumbi pamitu pao, nafuula, ndi kulira, ndi kuchita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, chifukwa cha kulemera kwake, pakuti mu ora limodzi unasanduka bwinja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa