Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 6:12 - Buku Lopatulika

12 Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mmodzi mwa aphunguwo adayankha kuti, “Palibe ndi mmodzi yemwe, inu mbuyanga mfumu. Koma Elisa mneneri wa ku Israele ndiye amene amauza mfumu ya ku Israele mau amene inuyo mumalankhula kumbali m'chipinda mwanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mmodzi mwa atsogoleri a ankhondowo anati, “Palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu, inu mbuye wanga, koma Elisa mneneri amene ali ku Israeli amawuza mfumu ya ku Israeli mawu enieni amene inu mumayankhula ku chipinda kwanu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 6:12
19 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeze kodi, umo munthuyo anatembenuka pa galeta wake kukomana ndi iwe? Kodi nyengo ino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zovala, ndi minda ya azitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi akapolo, ndi adzakazi?


Nati uyu kwa mbuyake wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali mu Samariya, akadamchiritsa khate lake.


Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israele adang'amba zovala zake, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zovala zanu chifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israele.


Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?


Nati iye, Kamuoneni komwe ali; ndikatume munthu kumtenga. Ndipo anamuuza kuti, Ali ku Dotani.


ndipo m'mtsinjemo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'michembo yanu yootcheramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo.


Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife?


Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.


Mfumu inamyankha Daniele, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi.


Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa