2 Mafumu 5:8 - Buku Lopatulika8 Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israele adang'amba zovala zake, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zovala zanu chifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israele adang'amba zovala zake, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zovala zanu chifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri m'Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Koma mneneri Elisa atamva kuti mfumu ya ku Israele idang'amba zovala zake, adatumiza mau kwa mfumuyo akuti, “Chifukwa chiyani mwang'amba zovala zanu? Alendowo abwere kwa ine tsopano lino, kuti adziŵe kuti ku Israele kuli mneneri.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Elisa munthu wa Mulungu atamva kuti mfumu ya ku Israeli yangʼamba mkanjo wake, anatumiza uthenga uwu: “Chifukwa chiyani mwangʼamba mkanjo wanu? Mutumizeni munthuyo kwa ine ndipo iyeyo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israeli.” Onani mutuwo |
Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.