Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 5:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo anafika kwa mfumu ya Israele ndi kalata, yakuti, Pakulandira kalata iyi, taonani, ndatumiza Naamani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumchiritse khate lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo anafika kwa mfumu ya Israele ndi kalata, wakuti, Pakulandira kalata uyu, taonani, ndatumiza Naamani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumchiritse khate lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Atafika kwa mfumu ya ku Israele, adapereka kalata ija imene mau ake anali akuti, “Landirani kalatayi. Tsono amene ndakutumiziraniyo ndi Naamani mtumiki wanga, ndipo ndikufuna kuti inuyo mumchize khate lake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kalata imene anapita nayo kwa mfumu ya ku Israeli inali ndi mawu awa: “Taonani, ndikutumiza Naamani mtumiki wanga pamodzi ndi kalatayi kwa inu kuti mumuchiritse khate lake.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 5:6
3 Mawu Ofanana  

Tsono ikakufikani inu kalata iyi, popeza muli nao ana a mbuye wanu, muli naonso magaleta ndi akavalo, ndi mizinda yalinga, ndi zida,


Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israele. Pamenepo anachoka, atatenga siliva matalente khumi, ndi golide masekeli zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zovala zakusintha khumi.


Ndipo kunali atawerenga kalatayo mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa