Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 5:5 - Buku Lopatulika

5 Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israele. Pamenepo anachoka, atatenga siliva matalente khumi, ndi golide masekeli zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zovala zakusintha khumi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israele. Pamenepo anachoka, atatenga siliva matalente khumi, ndi golide masekeli zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zovala zakusintha khumi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pamenepo mfumuyo idamuuza kuti, “Ai ndithu upite, ine ndilemba kalata yofotokozera kwa mfumu ya ku Israele.” Choncho Naamani adanyamuka ulendo wopita ku Samariya, atatenga ndalama zasiliva 30,000, ndalama zagolide 6,000, ndiponso zovala khumi zapachikondwerero.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mfumu ya ku Aramu inayankha kuti, “Iwe uyenera kupita. Ine ndilembera kalata mfumu ya ku Israeli.” Choncho Naamani ananyamuka kupita ku Samariya, atatenga ndalama za siliva 30,000, ndalama zagolide 6,000 ndiponso zovala khumi za pa chikondwerero.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 5:5
21 Mawu Ofanana  

Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.


Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake.


Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa masekeli a siliva mazana atatu ndi zovala zopindula zisanu.


Mfumu niti kwa munthu wa Mulungu, Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso.


Ndipo mfumu ya Israele ananena ndi anyamata ake, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Giliyadi ngwathu, ndipo tangokhala chete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu.


Ndipo anadza munthu kuchokera ku Baala-Salisa, nabwera nayo m'thumba mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye.


Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti.


Ndipo anafika kwa mfumu ya Israele ndi kalata, yakuti, Pakulandira kalata iyi, taonani, ndatumiza Naamani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumchiritse khate lake.


Mtulo wa munthu umtsegulira njira, numfikitsa pamaso pa akulu.


Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe.


Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wampesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi;


Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.


Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao;


Nanena nao Samisoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kumasulira uwu, ndidzakupatsani malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa