2 Mafumu 5:23 - Buku Lopatulika23 Nati Naamani, Ulole ulandire matalente awiri. Namkakamiza namanga matalente awiri a siliva m'matumba awiri, ndi zovala zosintha ziwiri, nasenzetsa anyamata ake awiri; iwo anatsogola atazisenza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Nati Naamani, Ulole ulandire matalente awiri. Namkakamiza namanga matalente awiri a siliva m'matumba awiri, ndi zovala zosintha ziwiri, nasenzetsa anyamata ake awiri; iwo anatsogola atazisenza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Pamenepo Naamani adati, “Inu tengani ndithu ngakhale 6,000 zimene.” Choncho adamkakamiza, nalonga m'matumba ndalama za silivazo, pamodzi ndi zovala zapaphwandozo, nasenzetsa antchito ake aŵiri. Ndipo adanyamuka, antchitowo patsogolo, Gehazi pambuyo pao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Naamani anati, “Kuli bwino utenge ndalama zasiliva 6,000.” Iye anakakamiza Gehazi kuti alandire, ndipo kenaka anamanga matumba awiri a ndalama zasiliva pamodzi ndi zovala zinayi za pa mphwando. Naamani anazipereka kwa antchito ake awiri ndipo anazinyamula nayenda patsogolo pa Gehazi. Onani mutuwo |