2 Mafumu 5:22 - Buku Lopatulika22 Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ochokera ku mapiri a Efuremu; muwapatse talente wa siliva, ndi zovala zosintha ziwiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ochokera ku mapiri a Efuremu; muwapatse talente wa siliva, ndi zovala zosintha ziwiri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Gehazi adati, “Inde, nkwabwino. Koma mbuyanga wandituma chifukwa tsopano apa kwangomufikira anthu aŵiri a m'gulu la aneneri, kuchokera ku dziko lamapiri la Efuremu. Tsono akukupemphani kuti chonde muŵapatseko ndalama zasiliva 3,000 ndi zovala ziŵiri zapaphwando.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Gehazi anayankha kuti, “Inde nʼkwabwino. Mbuye wanga wandituma kuti ndidzakuwuzeni kuti, ‘Anyamata awiri mwa ana a aneneri angondipeza kumene kuchokera ku dziko la mapiri la Efereimu. Chonde apatseniko ndalama za siliva 3,000 ndi zovala ziwiri za pa phwando.’ ” Onani mutuwo |