Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 5:12 - Buku Lopatulika

12 Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a mu Israele? Ndilekerenji kukasamba m'mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nachoka molunda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a m'Israele? Ndilekerenji kukasamba m'mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nachoka molunda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko, siposa mitsinje yonse ya ku Israele kuno? Monga sindikadatha kukasamba m'mitsinje imeneyo ndi kuchiritsidwa?” Pomwepo adapotoloka, nachokapo molunda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko, siyoposa mitsinje ina yonse ya ku Israeli? Kodi sindikanasamba mʼmitsinje imeneyo ndi kuyeretsedwa?” Kotero anatembenuka nachoka ali wokwiya kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 5:12
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga chofunda cha Eliya chidamtayikiracho, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.


Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.


Koma Naamani adapsa mtima, nachoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kutuluka adzanditulukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wake, ndi kuweyula dzanja lake pamalopo, ndi kuchiritsa wakhateyo.


Ndipo Naamani anati, Mukakana, andipatse akatundu a dothi osenza nyuru ziwiri; pakuti mnyamata wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu ina, koma kwa Yehova.


Wokangaza kukwiya adzachita utsiru; ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.


Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mzinda.


Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.


Idza nane kuchokera ku Lebanoni, mkwatibwi, kuchokera nane ku Lebanoni: Unguza pamwamba pa Amana, pansonga ya Seniri ndi Heremoni, pa ngaka za mikango, pa mapiri a anyalugwe.


Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete.


Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala mu Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lao lina kunka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kunka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.


Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane mu Yordani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa