2 Mafumu 4:43 - Buku Lopatulika43 Koma mnyamata wake anati, Chiyani? Ndigawire amuna zana ichi kodi? Koma anati, Uwapatse anthu kuti adye; pakuti atero Yehova, Adzadya nadzasiyako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201443 Koma mnyamata wake anati, Chiyani? Ndigawire amuna zana ichi kodi? Koma anati, Uwapatse anthu kuti adye; pakuti atero Yehova, Adzadya nadzasiyako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa43 Koma wantchito wake adamufunsa kuti, “Kodi chakudya chimenechi ndingachigaŵe motani kwa anthu 100 onseŵa?” Elisayo adanenanso kuti, “Apatseni anthuwo, pakuti Chauta akunena kuti, ‘Anthuwo adzadya ndipo chakudyacho chidzatsalako.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero43 Mtumiki wake anafunsa kuti, “Kodi ndikachigawe motani chakudyachi kwa anthu 100?” Koma Elisa anamuwuzanso kuti, “Apatse anthu adye. Pakuti izi ndi zimene Yehova akunena kuti, ‘Iwo adzadya chakudyachi ndipo china chidzatsalako.’ ” Onani mutuwo |